9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,Ndinu wokwezeka kwakukuru pamwamba pa milungu yonse yina.
10 Inuokonda Yehova, danani naco coipa:Iye asunga moyo wa okondedwa ace;Awalanditsa m'manja mwa oipa.
11 Kuunika kufesekera wolungama, Ndi cikondwerero oongoka mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.