1 Ndidzayimba za cifundo ndi ciweruzo;Ndidzayimba zakukulemekezani Inu, Yehova.
2 Ndidzacita mwanzeru m'njira yangwiro;Mudzandidzera liti?Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3 Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga;Cocita iwo akupatuka padera cindiipira;Sicidzandimamatira.
4 Mtima wopulukira udzandicokera;Sindidzadziwana naye woipa.
5 Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.