3 Sindidzaika cinthu coipa pamaso panga;Cocita iwo akupatuka padera cindiipira;Sicidzandimamatira.
4 Mtima wopulukira udzandicokera;Sindidzadziwana naye woipa.
5 Wakuneneza mnzace m'tseri ndidzamdula;Wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;Iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
7 Wakucita cinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;Wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.
8 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko;Kuduliratu onse akucita zopanda pace ku mudzi wa Yehova.