3 Akapasuka maziko,Wolungama angacitenji?
4 Yehova ali m'Kacisi wace woyera,Yehova, mpando wacifumu wace uli m'Mwamba;Apenyerera ndi maso ace, ayesa ana a anthu ndi zikope zace.
5 Yehova ayesa wolungama mtima:Koma moyo wace umuda woipa ndi iye wakukonda ciwawa.
6 Adzagwetsa pwata pwata misampha pa oipa;Moto ndi miyala yasuifure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'cikho cao.
7 Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama:Woongoka mtima adzapenya nkhope yace.