3 Cocita Iye nca ulemu, ndi ukuru:Ndi cilungamo cace cikhalitsa kosatha.
4 Anacita cokumbukitsa zodabwiza zace;Yehova ndiye wa cisomo ndi nsoni zokoma.
5 Anapatsa akumuopa Iye cakudya;Adzakumbukila cipangano cace kosatha.
6 Anaonetsera anthu ace mphamvu ya nchito zace,Pakuwapatsa colowa ca amitundu.
7 Nchito za manja ace ndizo caonadi ndi ciweruzo;Malangizo ace onse ndiwo okhulupirika.
8 Acirikizika ku nthawi za nthawi,Acitika m'coonadi ndi cilunjiko,
9 Anatumizira anthu ace cipulumutso;Analamulira cipangano cace kosatha;Dzina lace ndilo loyera ndi loopedwa.