7 Nchito za manja ace ndizo caonadi ndi ciweruzo;Malangizo ace onse ndiwo okhulupirika.
8 Acirikizika ku nthawi za nthawi,Acitika m'coonadi ndi cilunjiko,
9 Anatumizira anthu ace cipulumutso;Analamulira cipangano cace kosatha;Dzina lace ndilo loyera ndi loopedwa.
10 Kumuopa Yehova ndiko ciyambi ca nzeru;Onse akucita cotero ali naco cidziwitso cokoma;Cilemekezo cace cikhalitsa kosatha.