1 Haleluya;Lemekezani, inu atumiki a Yehova;Lemekezani dzina la Yehova,
2 Lodala dzina la Yehova.Kuyambira tsopano kufikira kosatha.
3 Citurukire dzuwa kufikira kulowa kwaceLilemekezedwe dzina la Yehova.
4 Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,Ulemerero wace pamwambamwamba.