1 Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, Koma kwa dzina lanu patsani ulemerero,Cifukwa ca cifundo canu, ndi coonadi canu.
2 Aneneranji amitundu,Ali kuti Mulungu wao?
3 Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba;Acita ciri conse cimkonda.
4 Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi,Nchito za manja a anthu.