155 Cipulumutso citalikira oipa;Popeza safuna malemba anu.
156 Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova;Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.
157 Ondilondola ndi ondisautsa ndiwoambiri;Koma sindinapatukana nazo mboni zanu.
158 Ndinapenya ocita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;Popeza sasamalira mau anu.
159 Penyani kuti ndikonda malangizo anu;Mundipatse moyo, Yehova, monga mwa cifundo canu.
160 Ciwerengero ca mau anu ndico coonadi;Ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161 Nduna zinandilondola kopanda cifukwa;Koma mtima wanga ucita mantha nao mau anu.