160 Ciwerengero ca mau anu ndico coonadi;Ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161 Nduna zinandilondola kopanda cifukwa;Koma mtima wanga ucita mantha nao mau anu.
162 Ndikondwera nao mau anu,Ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.
163 Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;Koma ndikonda cilamulo canu.
164 Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,Cifukwa ca maweruzo anu alungama.
165 Akukonda cilamulo canu ali nao mtendere wambiri;Ndipo alibe cokhumudwitsa.
166 Ndinayembekeza cipulumutso canu, Yehova,Ndipo ndinacita malamulo anu.