29 Mundicotsere njira ya cinyengo;Nimundipatse mwacifundo cilamulo canu.
30 Ndinasankha njira yokhulupirika;Ndinaika maweruzo anu pamaso, panga,
31 Ndimamatika nazo mboni zanu;Musandicititse manyazi, Yehova.
32 Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,Mutakulitsa mtima wanga.
33 Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;Ndidzaisunga kufikira kutha kwace.
34 Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;Ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
35 Mundiyendetse mopita malamulo anu;Pakuti ndikondwera m'menemo.