35 Mundiyendetse mopita malamulo anu;Pakuti ndikondwera m'menemo.
36 Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu,Si ku cisiriro ai.
37 Mucititse mlubza maso anga ndisapenye zacabe,Mundipatse moyo mu njira yanu.
38 Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,Ndiye wodzipereka kukuopani.
39 Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco;Popeza maweruzo anu ndi okoma.
40 Taonani, ndinalira malangizo anu;Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.
41 Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova,Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.