4 Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani,Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu.
5 Ndipo adzayimbira njira za Yehova;Pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukuru.
6 Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo;Koma wodzikuza amdziwira kutali.
7 Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo;Mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu,Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
8 Yehova adzanditsirizira za kwa ine:Cifundo canu, Yehova, cifikira ku nthawi zonse:Musasiye nchito za manja anu.