1 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;
2 Amene adzipanga zoipa mumtima mwao;Masiku onse amemeza nkhondo.
3 Anola lilime lao ngati njoka;Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.
4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.