2 Amene adzipanga zoipa mumtima mwao;Masiku onse amemeza nkhondo.
3 Anola lilime lao ngati njoka;Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.
4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
5 Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe;Anacha ukonde m'mphepete mwa njira;Anandichera makwekwe.
6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga,Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.