4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
5 Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe;Anacha ukonde m'mphepete mwa njira;Anandichera makwekwe.
6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga,Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.
9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,Coipa ca milomo yao ciwaphimbe.
10 Makala amoto awagwere;Aponyedwe kumoto;M'maenje ozama, kuti asaukenso.