8 Ndisungeni monga kamwana ka m'diso,Ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,
9 Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,Adani a pa moyo wanga amene andizinga.
10 Mafuta ao awatsekereza;M'kamwa mwao alankhula modzikuza.
11 Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu:Apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.
12 Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,Ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.
13 Ukani Yehova,Mumtsekereze, mumgwetse:Landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
14 Kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,Kwa anthu a dziko lapansi pano amene colowa cao ciri m'moyo uno,Ndipo mimba yao muidzaza ndi cuma canu cobisika:Akhuta mtima ndi ana,Nasiyira ana amakanda zocuruka zao.