3 Atsitsimutsa moyo wanga;Anditsogolera m'mabande a cilungamo, cifukwa ca dzina lace.
4 Inde, ndingakhale ndiyenda m'cigwa ca mthunzi wa Imfa,Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine:Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,
5 Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga:Mwandidzoza mutu wanga mafuta; cikho canga cisefuka.
6 Inde ukoma ndi cifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga:Ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.