1 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zace zomwe,Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.
2 Pakuti Iye analimanga pazinyanja,Nalikhazika pamadzi.
3 Adzakwera ndani m'phiri la Yehova?Nadzaima m'malo ace oyera ndani?
4 Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye;Iye amene sanakweza moyo wace kutsata zacabe,Ndipo salumbira monyenga,