2 Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu,Ndisacite manyazi;Adani anga asandiseke ine.
3 Inde, onse akuyembekezera Inu sadzacita manyaziAdzacita manyazi iwo amene acita monyenga kopanda cifukwa.
4 Mundidziwitse njira zanu, Yehova;Mundiphunzitse mayendedwe anu.
5 Munditsogolere m'coonadi canu, ndipo mundiphunzitse;Pakuti Inu ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
6 Kumbukilani, Yehova, nsoni zanu ndi cifundo canu;Pakuti izi nza kale lonse,
7 Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu:Mundikumbukile monga mwa cifundo canu,Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova.
8 Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima:Cifukwa cace adzaphunzitsa olawa za njira.