8 Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima:Cifukwa cace adzaphunzitsa olawa za njira.
9 Adzawatsogolera ofatsa m'ciweruzo:Ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yace.
10 Mayendedwe onse a Yehova ndiwo cifundo ndi coonadi,Kwa iwo akusunga pangano lace ndi mboni zace.
11 Cifukwa ca dzina lanu, Yehova,Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.
12 Munthuyo wakuopa Yehova ndani?Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.
13 Moyo wace udzakhala mokoma;Ndi mbumba zace zidzalandira dziko lapansi.
14 Cinsinsi ca Yehova ciri kwa iwo akumuopa Iye;Ndipo adzawadziwitsa pangano lace.