1 Yehova ndiye kuunika kwanga ndi cipulumutso canga; ndidzaopa yani?Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzacita mantha ndi yani?
2 Pondifika ine ocita zoipa kudzadya mnofu wanga,Inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.
3 Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole,Mtima wanga sungacite mantha:Ingakhale nkhondo ikandiukira,Nde pomweponso ndidzakhulupira,
4 Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici:Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.
5 Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace:Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace;Pathanthwe adzandikweza.