6 Aitumphitsa monga mwana wa ng'ombe;Lebano ndi Sirio monga msona wa njati.
7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.
8 Liu la Yehova ligwedeza cipululu;Yehova agwedeza cipululu ca Kadese.
9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,Ndipo lipulula nkhalango:Ndipo m'Kacisi mwace zonse ziri m'mwemo zimati, Ulemerero:
10 Yehova anakhala pa Cigumula:Inde Yehova akhala mfumu ku nthawi yomka muyaya.
11 Yehova adzapatsa anthu ace mphamvu:Yehova adzadalitsa anthu ace ndi mtendere.