1 Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,Ndipo simunandikondwetsera adani anga,
2 Yehova, Mulungu wanga,Ndinapfuulira kwa Inu, ndipo munandiciritsa.
3 Yehova munabweza moyo wanga kumanda:Munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.
4 Yimbirani Yehova, inu okondedwa ace,Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.