2 Yehova, Mulungu wanga,Ndinapfuulira kwa Inu, ndipo munandiciritsa.
3 Yehova munabweza moyo wanga kumanda:Munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.
4 Yimbirani Yehova, inu okondedwa ace,Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.
5 Pakuti mkwiyo wace ukhala kanthawi kokha;Koma kuyanja kwace moyo wonse:Kulira kucezera,Koma mamawa kuli kupfuula kukondwera.
6 Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa,Sindidzagwedezeka nthawi zonse.
7 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu:Munabisa nkhope yanu; ndinaopa.
8 Ndinapfuulira kwa Inu, Yehova;Kwa Yehova ndinapemba: