4 Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.
5 Ndinabvomera coipa canga kwa Inu;Ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa.Ndinati, Ndidzaululira Yehova macimo anga;Ndipo munakhululukira coipa ca kulakwa kwanga.
6 Cifukwa cace oyera mtima onse apemphere kwa Inu,Pa nthawi ya kupeza Inu:Indetu pakusefuka madzi akuruSadzamfikira iye.
7 Inu ndinu mobisalira mwanga; M'nsautso mudzandisunga;Mudzandizinga ndi Nyimbo za cipulumutso.
8 Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo;Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
9 Musakhale monga kavalo, kapena ngati buru, wopanda nzeru:Zomangira zao ndizo cam'kamwa ndi capamutu zakuwakokera,Pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.
10 Zisoni zambiri zigwera woipa:Koma cifundo cidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.