4 Athe nzeru nacite manyazi iwo akufuna moyo wanga:Abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira ciwembu.
5 Akhale monga mungu kumphepo,Ndipo mngelo wa Yehova awapitikitse.
6 Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera,Ndipo mngelo wa Yehova awalondole.
7 Pakuti anandichera ukonde wao m'mbunamo kopanda cifukwa,Anakumbira moyo wanga dzenje kopanda cifukwa.
8 Cimgwere modzidzimutsa cionongeko;Ndipo ukonde wace umene anaucha umkole yekha mwini:Agwemo, naonongeke m'mwemo.
9 Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova:Udzasekera mwa cipulumutso cace.
10 Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani,Wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu,Ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?