3 Mau a pakamwa pace ndiwo opanda pace ndi onyenga:Waleka kuzindikira ndi kucita bwino.
4 Alingirira zopanda pace pakama pace;Adziika panjira posad pabwino;Coipa saipidwa naco.
5 Yehova, m'mwambamuli cifundo canu;Coonadi canu cifikira kuthambo.
6 Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:Yehova, musunga munthu ndi nyama.
7 Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.
8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu:Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.
9 Pakuti citsime ca moyo ciri ndi Inu:M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.