6 Cilungamo canu cikunga mapiri a Mulungu;Maweruzo anu akunga cozama cacikuru:Yehova, musunga munthu ndi nyama.
7 Ha! cifundo canu, Mulungu, ncokondedwadi!Ndipo ana a anthu athawira ku mthunzi wa mapiko anu.
8 Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu:Ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.
9 Pakuti citsime ca moyo ciri ndi Inu:M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.
10 Tanimphitsani cifundo canu pa iwo akudziwa Inu;Ndi cilungamo canu pa oongoka mtima.
11 Phazi la akudzikuza lisandifikire ine,Ndi dzanja la oipa lisandicotse.
12 Pomwepo padagwera ocita zopanda pace:Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.