28 Pakuti Yehova akonda ciweruzo,Ndipo sataya okondedwa ace:Asungika kosatha:Koma adzadula mbumba za oipa.
29 Olungama adzalandira dziko lapansi,Nadzakhala momwemo kosatha.
30 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,Ndi lilime lace linena ciweruzo.
31 Malamulo a Mulungu wace ali mumtima mwace;Pakuyenda pace sadzaterereka.
32 Woipa aunguza wolungama,Nafuna kumupha.
33 Yehova sadzamsiya m'dzanja lace:Ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.
34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yace,Ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko:Pakudutidwa oipa udzapenya,