33 Yehova sadzamsiya m'dzanja lace:Ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.
34 Yembekeza Yehova, nusunge njira yace,Ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko:Pakudutidwa oipa udzapenya,
35 Ndapenya woipa, alikuopsa,Natasa monga mtengo wauwisi wanzika.
36 Koma anapita ndipo taona, kwati zi:Ndipo ndinampwaira osampeza.
37 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!Pakuti ku matsiriziro ace a munthuyo kuti mtendere.
38 Koma olakwa adzaonongeka pamodzi:Matsiriziro a oipa adzadutidwa.
39 Koma cipulumutso ca olungama cidzera kwa Yehova,Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.