5 Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga.
6 Ndapindika, ndawerama kwakukuru;Ndimayenda woliralira tsiku lonse.
7 Pakuti m'cuuno mwanga mutentha kwambiri;Palibe pamoyo m'mnofu mwanga,
8 Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa:Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga.
9 Ambuye, cikhumbo canga conse ciri pamaso panu;Ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.
10 Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yacoka:Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandicokera.
11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;Ndipo anansi anga aima patali.