3 Onse anabwerera; anabvunda mtima pamodzi;Palibe mmodzi wakucita bwino, nnena mmodzi.
4 Kodi ocita zopanda pace sadziwa?Pomadya anthu anga monga akudya mkate;Ndipo saitana Mulungu.
5 Pamenepo anaopa kwakukuru, popanda cifukwa ca kuopa:Pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;Unawacititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
6 Ha, cipulumutso ca Israyeli cicokere m'Ziyoni!Pakubweretsa Mulungu anthu ace a m'ndende,Yakobo adzakondwera, Israyeli adzasekera.