1 Cherani khutu pemphero langa, Mulungu;Ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga.
2 Mveram, ndipo mundiyankhe:Ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula;
3 Cifukwa ca mau a mdani,Cifukwa ca kundipsinja woipa;Pakuti andisenza zopanda pace,Ndipo adana nane mumkwiyo.
4 Mtima wanga uwawa m'kati mwanga;Ndipo zoopsa za imfa zandigwera.
5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,Ndipo zoopsetsa zandikuta.