3 Cifukwa ca mau a mdani,Cifukwa ca kundipsinja woipa;Pakuti andisenza zopanda pace,Ndipo adana nane mumkwiyo.
4 Mtima wanga uwawa m'kati mwanga;Ndipo zoopsa za imfa zandigwera.
5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,Ndipo zoopsetsa zandikuta.
6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwaMwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
7 Onani, ndikadathawira kutari,Ndikadagona m'cipululu.
8 Ndikadafulumira ndipulumukeKu mphepo yolimba ndi namondwe.
9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.