14 Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,Nazungulire mudzi.
15 Ayendeyende ndi kufuna cakudya,Nacezere osakhuta.
16 Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu;Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa:Pakuti Inu mwakhala msanje wanga,Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
17 Ndidzayimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga:Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa cifundo canga.