6 Abwera madzulo, auwa ngati garu,Nazungulira mudzi.
7 Onani abwetuka pakamwa pao;M'milomo mwao muli lupanga,Pakuti amati, Amva ndani?
8 Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;Mudzalalatira amitundu onse.
9 Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.
10 Mulungu wa cifundo canga adzandikumika:Adzandionetsa tsoka la adani anga.
11 Musawapheretu, angaiwale anthu anga:Muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,Ambuye, ndinu cikopa cathu.
12 Pakamwa pao acimwa ndi mau onse a pa milomo yao,Potero akodwe m'kudzitamandira kwao,Ndiponso cifukwa ca kutemberera ndi bodza azilankhula.