1 Imvani mpfuu wanga, Mulungu;Mverani pemphero langa.
2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga:Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m'kutalika kwace.
3 Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pathawa mdani ine.
4 Ndidzagonera-gonerabe m'cihemamwanu;Ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.