2 Ku malekezero a dziko lapansi ndidzapfuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga:Nditsogolereni ku thanthwe londiposa ine m'kutalika kwace.
3 Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pathawa mdani ine.
4 Ndidzagonera-gonerabe m'cihemamwanu;Ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.
5 Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga;Munandipatsa colowa ca iwo akuopa dzina lanu.
6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu:Zaka zace zidzafikira mibadwo mibadwo.
7 Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu;Mumpatse cifundo ndi coonadi zimsunge.
8 Potero ndidzayimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse,Kuti ndicite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.