12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa:Ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.
13 Pogona inu m'makola a zoweta,Mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva,Ndi nthenga zace zokulira ndi golidi woyenga wonyezimira.
14 Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo,Munayera ngati matalala m'Salimoni.
15 Phiri la Basana ndilo phiri la Mulungu;Phiri la Basana ndilo phiri la mitu mitu.
16 Mucitiranji nsanje mapiri inu a mitu mitu,Ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko?Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha.
17 Magareta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikiza-wirikiza:Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika,
18 Munakwera kumka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende;Munalandira zaufulu mwa anthu,Ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.