4 Ondida kopanda cifukwa acuruka koposa tsitsi la pamutu panga;Ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu:Pamenepo andibwezetsa cosafunkha ine.
5 Mulungu, mudziwa kupusa kwanga;Ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu.
6 Iwo akuyembekeza Inu, Ambuve Yehova wa makamu, asacite manyazi cifukwa ca ine:Iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israyeli, asapepulidwe cifukwa ca ine.
7 Pakuti ndalola cotonza cifukwa ca Inu:Cimpepulo cakuta nkhope yanga,
8 Abale anga andiyesa mlendo,Ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina.
9 Pakuti cangu ca pa nyumba yanu candidya;Ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
10 Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga,Koma uku kunandikhalira cotonza.