1 Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu:Mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
2 Kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango,Ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.
3 Yehova Mulungu wanga, ngati ndacita ici;Ngati m'manja anga muli cosalungama;
4 Ngati ndambwezera coipa iye woyanjana ndine;(Inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda cifukwa);
5 Mdani alondole moyo wanga, naupeze;Naupondereze pansi moyo wanga,Naukhalitse ulemu wanga m'pfumbi.
6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,Nyamukani cifukwa ca ukali wa akundisautsa:Ndipo mugalamukire ine; mwalamulira ciweruzo.
7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;Ndipo pamwamba pao mubwerere kumka kumwamba.