4 Ngati ndambwezera coipa iye woyanjana ndine;(Inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda cifukwa);
5 Mdani alondole moyo wanga, naupeze;Naupondereze pansi moyo wanga,Naukhalitse ulemu wanga m'pfumbi.
6 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu,Nyamukani cifukwa ca ukali wa akundisautsa:Ndipo mugalamukire ine; mwalamulira ciweruzo.
7 Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu;Ndipo pamwamba pao mubwerere kumka kumwamba.
8 Yehova aweruza anthu mlandu:Mundiweruze, Yehova, monga mwa cilungamo canga, ndi ungwiro wanga uli mwa ine.
9 Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse:Pakuti woyesa mitima ndi imso ndiye Mulungu wolungama.
10 Cikopa canga ciri ndi Mulungu, Wopulumutsa oongoka mtima.