2 Acite manyazi, nadodomeAmene afuna moyo wanga:Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe.Amene akonda kundicitira coipa,
3 Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi aoAmene akuti, Hede, hede.
4 Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu;Nanene kosalekeza iwo akukonda cipulumutso canu,Abuke Mulungu.
5 Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi;Mundifulumirire, Mulungu:Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga;Musacedwe, Yehova.