1 Ndikhulupirira Inu, Yehova:Ndisacite manyazi nthawi zonse.
2 Ndikwatuleni m'cilungamo canu, ndi kundilanditsa:Ndicherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;Mwalamulira kundipulumutsa;Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
4 Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,M'dzanja la munthu wosalungama ndi waciwawa.
5 Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova;Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.