4 Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,M'dzanja la munthu wosalungama ndi waciwawa.
5 Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova;Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
6 Inu munandigwirizizakuyambira ndisanabadwe:Kuyambira pa thupi la mai wanga wondicitira zokoma ndinu;Ndidzakulemekezani kosalekeza.
7 Ndikhala codabwiza kwa ambiri;Koma Inu ndinu pothawira panga polimba.
8 M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,Ndi ulemu wanu tsiku lonse.
9 Musanditaye mu ukalamba wanga;Musandisiye, pakutha mphamvu yanga.
10 Pakuti adani anga alankhula za ine;Ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,