7 Pakuti Mulungu ndiye woweruza;Acepsa wina, nakuza wina.
8 Pakuti m'dzanja la Yehova muli cikho;Ndi vinyo wace acita thobvu;Cidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako:Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwaNadzagugudiza nsenga zace.
9 Koma ine ndidzalalikira kosalekeza,Ndidzayimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10 Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa;Koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.