4 Takhala cotonza ca anansi athu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga,
5 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?
6 Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,Ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.
7 Pakuti anathera Yakobo,Napasula pokhalira iye.
8 Musakumbukile moritsutsa mphulupulu za makolo athu;Nsoni zokoma zanu zitikumike msanga:Pakuti tafoka kwambiri.
9 Tithandizeni Mulungu wa cipulumutso cathu,Cifukwa ca ulemerero wa dzina lanu;Ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,Cifukwa ca dzina lanu.
10 Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao?Kubwezera cilango ca mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsaKudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu,