4 Pakuti ici ndi colemba ca kwa Israyeli,Ciweruzo ca Mulungu wa Yakobo.
5 Anaciika cikhale mboni kwa Yosefe,Pakuturuka iye ku dziko la Aigupto:Komwe ndinamva cinenedwe cosadziwa ine.
6 Ndinamcotsera katundu paphewa pace:Manja ace anamasuka kucotengera.
7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;Ndinakubvomereza mobisalika m'bingu;Ndinakuyesa ku madzi a Meriba.
8 Tamvani, anthu anga, ndidzakucitirani mboni;Israyeli, ukadzandimvera!
9 Kwanu kusakhale mulungu wafuma kwina;Nusagwadire mulungu wacilendo.
10 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukucotsa ku dziko la Aigupto;Yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.