6 Ndinamcotsera katundu paphewa pace:Manja ace anamasuka kucotengera.
7 Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;Ndinakubvomereza mobisalika m'bingu;Ndinakuyesa ku madzi a Meriba.
8 Tamvani, anthu anga, ndidzakucitirani mboni;Israyeli, ukadzandimvera!
9 Kwanu kusakhale mulungu wafuma kwina;Nusagwadire mulungu wacilendo.
10 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukucotsa ku dziko la Aigupto;Yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
11 Koma anthu anga sanamvera mau anga;Ndipo Israyeli sanandibvomera.
12 Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,Ayende monga mwa uphungu wao wao.